Exodus 7:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono amatsenga a ku Ejipito aja nawonso adachita zomwezo mwa matsenga ao, ndipo Farao adakhalabe wokanika. Sadamvere zimene ankanena Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo alembi a Aejipito anachita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvere iwo; monga adalankhula Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo alembi a Aigupto anacita momwemo ndi matsenga ao; koma mtima wa Farao unalimba, ndipo sanamvera iwo; monga adalankhula Yehova.