Exodus 7:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Faraoyo sadzakumverani. Pamenepo ndidzakantha dzikolo, ndipo pochita ntchito zamphamvu, ndidzatsogolera magulu anga, anthu anga Aisraele, kuŵatulutsa ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo akulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
iyeyo sadzakumverani. Choncho ndidzakantha Igupto, ndipo ndi ntchito zachiweruzo ndidzatulutsa magulu anga, anthu anga Aisraeli kuwachotsa mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aigupto, ndipo ndidzaturutsa makamu anga, anthu anga ana a Israyeli, m'dziko la Aigupto ndi maweruzo akuru.