Exodus 7:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ngati Farao akulamulani kuti, ‘Chitani chozizwitsa kuti tikukhulupirireni,’ iwe Mose ukauze Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao kuti isanduke njoka.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzichitireni chodabwitsa; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke chinjoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ngati Farao adzati kwa inu, ‘Chitani chozizwitsa,’ iwe Mose udzati kwa Aaroni, ‘Tenga ndodo yako ndipo uyiponye pamaso pa Farao,’ ndipo idzasanduka njoka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene Farao adzalankhula nanu, ndi kuti, Dzicitireni codabwiza; pamenepo uzinena ndi Aroni, Tenga ndodo yako, Iponye pansi pamaso pa Farao, isanduke cinjoka,