Exodus 8:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Farao ataona kuti zinthu zayamba kukhala bwino, adaumitsa mtima wake, ndipo sadafunenso kumvera Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Farao ataona kuti zinthu zinayambanso kukhala bwino, anawumitsanso mtima wake ndipo sanamverenso mawu a Mose ndi Aaroni, monga momwe Yehova ananenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pamene Farao, anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wace, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.