Exodus 8:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Chauta adalamula Mose kuti, “Uza Aroni asamule ndodo yake ndipo amenye nthaka, motero fumbi lonse lidzasanduka nthata m'dziko lonse la Ejipito.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti akweze ndodo yake ndi kumenya fumbi la pa nthaka, ndipo fumbilo lidzasanduka nsabwe pa dziko lonse la Igupto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande pfumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Aigupto.