Exodus 8:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwowo adachitadi momwemo. Aroni adasamula ndodo yake ija namenya nthaka. Tsono fumbi lonse lidasanduka nthata, ndipo zidabalalikira pa anthu ndi pa nyama zomwe. Motero fumbi lonse la ku Ejipito lidangokhala nthata zokhazokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anachita chomwecho; pakuti Aroni anasamula dzanja lake ndi ndodo yake, napanda fumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; fumbi lonse lapansi linasanduka nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anachita momwemo, ndipo pamene Aaroni anakweza ndodo yake ndi kumenya fumbi, nsabwe zinafika pa munthu aliyense ndi pa ziweto. Fumbi lonse la mʼdziko la Igupto linasanduka nsabwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anacita comweco; pakuti Aroni anasamula dzanja lace ndi ndodo yace, napanda pfumbi lapansi, ndipo panali nsabwe pa anthu ndi pa zoweta; pfumbi lonse lapansi liinasanduka nsabwe m'dziko lonse la Aigupto.