Exodus 8:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amatsenga aja adayesanso momwemo mwa matsenga ao kuti apange zao nthata, koma adalephera. Ndipo nthatazo zidabalalikira pa anthu ndi nyama zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoza; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma amatsenga atayesa kupanga nsabwe mwa matsenga awo, analephera. Ndipo nsabwezo zinali pa munthu aliyense ndi pa ziweto zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Alembi anateronso ndi matsenga ao kuonetsa nsabwe, koma sanakhoza; ndipo panali nsabwe pa anthu, ndi pa zoweta.