Exodus 8:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Chauta adauza Mose kuti “Maŵa m'maŵa ndithu, upite ukakumane ndi Farao pamene akupita ku mtsinje, ukamuuze kuti, ‘Chauta akunena kuti uŵalole anthu anga apite, akandipembedze Ine.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, atuluka kunka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uuke ulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao; taona, aturuka kumka kumadzi; nunene naye, Atero Yehova, Lola anthu anga amuke, anditumikire.