Exodus 8:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ukapanda kulola anthu anga kuti apite, ndidzatumiza mizaza pa iwe, nduna zako, anthu ako ndi m'nyumba mwako. M'nyumba zonse za Aejipito, ngakhalenso pa nthaka yonse imene akukhalapo, padzakhala mizaza yokhayokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati suwalola anthu anga kuti apite, Ine ndidzatumiza pa iwe ntchentche zoluma ndi pa nduna zako ndi anthu ako ndi mʼnyumba zanu. Mʼnyumba za Aigupto mudzadzaza ntchentche zoluma. Ngakhale pa nthaka pamene akhalapo padzadzaza ndi ntchentche zoluma.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aaigupto zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.