Exodus 8:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Chauta adachitadi zimenezi, ndipo magulu a mizaza adaloŵa m'nyumba ya Farao, m'nyumba za nduna zake, ndiponso m'dziko lonse la Ejipito. Dziko lonselo lidaipiratu ndi mizazayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anachita chomwecho; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ake, ndi m'dziko lonse la Ejipito; dziko linaipatu chifukwa cha mizazayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anachita zimenezi: Ntchentche zoluma zochuluka zinalowa mʼnyumba yaufumu ya Farao ndi nyumba za nduna zake. Choncho ntchentche zolumazi zinawononga dziko lonse la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehovaanacita comweco; ndipo kunafika magulu a mizaza m'nyumba ya Farao, ndi m'nyumba za anyamata ace, ndi m'dziko lonse la Aigupto; dziko linaipatu cifukwa ca mizazayo.