Exodus 8:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mose adayankha kuti, “Sikungakhale bwino konse kuchita zimenezo, chifukwa Aejipito zidzaŵaipira nsembe zimene timapereka kwa Chauta, Mulungu wathu. Tikadzapereka nsembe zimene Aejipito zimaŵanyansa m'maso mwao, kodi iwo sadzatiponya miyala mpaka kutipha?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu chonyansa cha Aejipito; taonani, ngati tikamphera nsembe chonyansa cha Aejipito pamaso pao sadzatiponya miyala kodi?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Mose anati, “Sitingathe kutero pakuti nsembe zathu kwa Yehova Mulungu ndi zowayipira Aigupto. Ngati tipereke nsembe zowayipira Aigupto mʼmaso mwawo, adzatiponya miyala kuti tife.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mose anati, Sikuyenera kutero; pakuti tidzamphera Yehova Mulungu wathu conyansa ca Aaigupto; taonani, ngati tikamphera nsembeconyansaca Aaigupto pamaso pao sadzatiponya miyala kodi?