Exodus 8:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Farao adati, “Ndidzakulolani kuti mupite mukapereke nsembe kwa Chauta, Mulungu wanu, ku chipululu, koma musapite kutali kwambiri. Tsono mundipempherere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m'chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao anati, “Ine ndikulolani kuti mupite ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu, koma musapite kutali kwambiri. Tsopano ndipempherereni.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova. Mulungu wanu m'cipululu; komatu musamuke kutaritu: mundipembere.