Exodus 8:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Mose adati, “Malinga ndikachoka pano, ndikukapempha kwa Chauta, ndipo maŵa mizaza ikuchokani inu, nduna zanu ndiponso anthu anu. Koma musatinyengenso ndi kuŵaletsa anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anayankha kuti, “Ine ndikangochoka pano, ndikapemphera kwa Yehova ndipo mawa lomweli ntchentche zoluma zidzachoka kwa Farao, nduna zake pamodzi ndi anthu ake. Koma Farao, onetsetsani kuti musachitenso zachinyengo ndi kuwakaniza anthu kuti asakapereke nsembe kwa Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mose anati, Onani, ndirikuturuka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza icoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ace, ndi kwa anthu ace; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.