Exodus 8:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Pomwepo mizaza idamchoka Farao ndi nduna zake ndi anthu ake omwe. Sudatsalepo ndi umodzi omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha: Ntchentche zoluma zinachoka kwa Farao ndi nduna zake ndiponso kwa anthu ake. Palibe ngakhale imodzi yomwe inatsala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anacita monga mwa mau a Mose; nacotsera Farao ndi anyamata ace ndi anthu ace mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse.