Exodus 8:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mose adauza Farao kuti, “Chabwino, mungondiwuza nthaŵi yoti ndikupempherereni inu, nduna zanu ndi anthu anu omwe, kuti achuleŵa akuchokeni, achokenso m'nyumba mwanu, ndipo kuti akakhale mumtsinje mokha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke achulewo, achokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'nyanja mokha?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mose anati kwa Farao, “Inu mungonditchulira nthawi imene mukufuna kuti ndikupempherereni, nduna zanu pamodzi ndi anthu anu kuti achule achoke mʼnyumba zanu ndi kuti atsale okhawo ali mu mtsinje wa Nailo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mose anati kwa Farao, Ulemu ndi wanu, wa ine ai; ndipembere inu ndi anyamata anu ndi anthu anu liti, kuti aonongeke aculewo, acokere inu ndi nyumba zanu, atsale m'nyanja mokha?