Exodus 9:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Chauta adauza Mose kuti, “Maŵa m'mamaŵa upite ukakumane ndi Farao, ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka nulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mawa mmawa upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso ndipo ukamuwuze kuti Yehova Mulungu wa Ahebri akuti ulole anthu anga apite kuti akandipembedze.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Uka oulawire mamawa, nuime pamaso pa Farao, nunene naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Lola anthu anga amuke, akanditumikire.