Exodus 9:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano lamula kuti zoŵeta zanu zonse zikhale m'khola pamodzi ndi zonse zimene muli nazo. Matalala adzagwa pa anthu ndi pa nyama zonse zongoyenda pa bwalo, chifukwa chosaziloŵetsa m'khola, ndipo zonsezo zidzafa.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano lamula kuti ziweto zanu zonse ndi zinthu zonse zomwe zili ku minda kuti zilowetsedwe mʼkhola, chifukwa matalala adzagwera munthu aliyense ndi chiweto chilichonse chimene sichidzalowetsedwa mʼkhola ndipo zimene zidzakhala zili ku munda zidzafa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, tumiza, thawitsa zoweta zako ndi zonse uli nazo pabwalo; pakuti anthu onse ndi zoweta zonse zopezeka pabwalo, zosasonkhanidwa m'nyumba, matalala adzazigwera, ndipo zidzafa.