Exodus 9:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nduna zina za Farao zidachita mantha chifukwa cha mau amene adanena Chauta, ndipo zidatsekera akapolo ao m'nyumba pamodzi ndi zoŵeta zao zomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ake ndi zoweta zake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nduna za Farao zinachita mantha ndi mawu a Yehova, ndipo zinalowetsa antchito awo ndi ziweto zawo mʼnyumba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iyeyu wa anyamata a Farao wakuopa mau a Yehova anathawitsira m'zinyumba anyamata ace ndi zoweta zace;