Exodus 9:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo panali mvula yamatalala ndi mphezi zong'anima kwambiri. Matalala ake anali oopsa kwambiri, kotero kuti chiyambire pamene Aejipito adasanduka mtundu wa anthu oima paokha, matalala otere sadagwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero panali matalala, ndi moto wakutsikatsika pakati pa matalala, choopsa ndithu; panalibe chotere m'dziko lonse la Ejipito chiyambire mtundu wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Matalala anagwa ndipo ziphaliwali zinangʼanima. Inali mphepo ya mkuntho yoopsa kwambiri imene sinakhaleponso mʼdziko lonse la Igupto chiyambire pamene Aigupto anakhala mtundu woyima pa okha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero panali matalala, ndi mota wakutsikatsika pakati pa matalala, coopsa ndithu; panalibe cotere m'dziko lonse la Aigupto ciyambire mtundu wao.