Exodus 9:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Matalalawo adaononga zonse zokhala panja m'dziko lonse la Ejipito, anthu onse pamodzi ndi nyama zomwe. Adaononganso zomera zonse zam'minda ndi kukadzulanso mitengo yonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Ejipito zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Matalala anawononga dziko lonse la Igupto, munthu aliyense pamodzi ndi ziweto. Matalala aja anawononga zomera zonse za mʼmunda ndi kukhadzula mtengo uliwonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo matalala anapanda m'dziko lonse la Aigupto zonse za pabwalo, kuyambira anthu kufikira zoweta; ndipo matalala anapanda zitsamba zonse za kuthengo, nathyola mitengo yonse ya kuthengo.