Exodus 9:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Zoonadi, ndachimwa ndithu tsopano. Chauta ndi wolungama, koma ineyo pamodzi ndi anthu anga, tonse ndife ochimwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndachimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati kwa iwo, “Tsopano ndachimwa, Yehova ndi wolungama, ine ndi anthu anga ndife olakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Farao anatumiza, naitana Mose ndi Aroni, nanena nao, Ndacimwa tsopano; Yehova ndiye wolungama, ine ndi anthu anga ndife oipa,