Exodus 9:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono m'maŵa mwake Chauta adachitadi monga momwe adanenera, ndipo zoŵeta zonse za Aejipito zidafa. Koma panalibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mawa mwake Yehova anachita chinthucho, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Ejipito; koma sichinafa chimodzi chonse cha zoweta za ana a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mmawa mwake Yehova anachitadi zimenezi. Ziweto zonse za Aigupto zinafa, koma palibe chiweto ndi chimodzi chomwe cha Aisraeli chomwe chinafa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mawa mwace Yehova anacita cinthuco, ndipo zinafa zoweta zonse za m'Aigupto; koma sicinafa cimodzi conse ca zoweta za ana a Israyeli.