Exodus 9:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Farao atafunsitsa zimene zidaachitikazo, adamva kuti palibe ndi chiŵeto nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo. Komabe Farao adakhala wokanika ndithu, ndipo sadalole konse kuti anthuwo apite.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafa chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Farao anatuma anthu kuti akafufuze ndipo anapeza kuti palibe chiweto chilichonse cha Aisraeli chomwe chinafa. Komabe mtima wake sunagonje ndipo iye sanalole kuti anthu apite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Farao anatuma, taonani, sicidafa cingakhale cimodzi comwe ca zoweta za Aisrayeli. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalola anthu amuke.