Ezekiel 1:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhope zake zinkaoneka motere: chilichonse chinali ndi nkhope zinai zosiyana. Kutsogolo nkhope ya munthu, ku dzanja lamanja nkhope ya mkango, ku dzanja lamanzere nkhope ya ng'ombe, ndipo kumbuyo kwake nkhope ya chiwombankhanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya kudzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya kudzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nkhope zawo zimaoneka motere: Chilichonse chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo mbali ya kumanja chilichonse chinali ndi nkhope zinayi zosiyana motere: nkhope ya munthu, nkhope ya mkango ku dzanja lamanja, nkhope ya ngʼombe ku dzanja lamanzere, ndipo kumbuyo kwake nkhope ya chiwombankhanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mafaniziro a nkhope zao zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya mkango pa mbali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinai zinali nayo nkhope ya ng'ombe pa mbali ya ku dzanja lamanzere; izi zinai zinali nayonso nkhope ya ciombankhanga.