Ezekiel 1:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakati pake pa zilengolengozo panali chinthu chooneka ngati makala oyaka, kapena ngati miyuni yoyaka yomangoyendayenda pakati pake. Motowo unali woŵala zedi, ndipo m'kati mwake munkatuluka mphezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makala amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unachita cheza, ndi m'motomo mudatuluka mphezi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakati pa zamayozo panali chinthu chooneka ngati makala oyaka kapena miyuni yoyaka. Moto umayendayenda pakati pa zamayozo; wowala kwambiri, ndipo mphenzi zimatuluka pakati pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kunena za mafaniziro a zamoyozo, maonekedwe ao ananga makara amoto, monga maonekedwe a miyuni; motowo unayendayenda pakati pa zamoyozo, ndi motowo unacita ceza, ndi m'motomo mudaturuka mphezi.