Ezekiel 1:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Maonekedwe a mikomberoyo anali onga a mwala wonyezimira, ndipo inai yonseyo inali yolingana. Mapangidwe ake anali ngati kuti mikomberoyo idaloŵanaloŵana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maonekedwe a mikomberoyo anali ngati mwala wonyezimira. Mikombero yonse inali yofanana ndipo mapangidwe awo anali ngati wongolowanalowana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maonekedwe a njingazi ndi mapangidwe ao ananga mawalidwe a berulo; ndi izi zinai zinafanana mafaniziro ao; ndi maonekedwe ao ndi mapangidwe ao anali ngati njinga ziwiri zopingasitsana.