Ezekiel 1:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zilengolengo zinkati zikamayenda, mikombero inkayendanso. Zilengolengo zikaima, mikombero inkaimanso. Zilengolengo zikauluka, mikombero inkauluka nazo pamodzi. Pakuti mzimu wa zilengolengozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izo; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izi; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zamoyo zija zinkati zikamayenda mikombero imayendanso. Zamoyozo zimati zikayima, nayonso mikombero inkayima. Zamoyozo zinkati zikawuluka, mikomberonso imawuluka nazo pamodzi chifukwa mzimu wa zamoyo zija ndiwo umayendetsa mikombero ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Poyenda zija zinayenda izi, poima zija zinaima izi; ndipo ponyamuka pansi zija njingazi zinanyamuka pambali pa izo; pakuti mzimu wa zamoyozo unali mu njingazi.