Ezekiel 1:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamwamba pa thambo lija panali chinthu china chooneka ngati mpando waufumu, wopangidwa ndi mwala wa safiro. Pamwamba pa mpandowo panali chinthu chooneka ngati munthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pamwamba pa thambolo linali pamitu pao panali chifaniziro cha mpando wachifumu, maonekedwe ake ngati mwala wa safiro; ndipo pa chifaniziro cha mpando wachifumu panali chifaniziro ngati maonekedwe ake a munthu wokhala pamwamba pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamwamba pa thambo la pa mitu yake panali chinthu chimene chimaoneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wa safiro, ndipo pamwamba pa mpando waufumuwo panali chinthu chooneka ngati munthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pamwamba pa thambo linali pamitu pao panali cifaniziro ca mpando wacifumu, maonekedwe ace ngati mwala wa safiro; ndipo pa cifaniziro ca mpando wacifumu panali cifaniziro ngati maonekedwe ace a munthu wokhala pamwamba pace.