Ezekiel 1:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'mwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo choŵala konsekonse ngati moto. M'munsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokhawo. Kuŵala kwamphamvu kudaamzungulira munthuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapenya ngati chitsulo chakupsa, ngati maonekedwe ake a moto m'kati mwake pozungulira pake, kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kumwamba kwake; ndipo kuyambira maonekedwe a m'chuuno mwake ndi kunsi kwake ndinaona ngati maonekedwe ake a moto; ndi kunyezimira kudamzinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinaona kuti mmwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo chowala konsekonse ngati moto. Mʼmunsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokha. Kuwala kwa mphamvu kunamuzungulira munthuyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapenya ngati citsulo cakupsa, ngati maonekedwe ace a moto m'kati mwace pozungulira pace, kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kumwamba kwace; ndipo kuyambira maonekedwe a m'cuuno mwace ndi kunsi kwace ndinaona ngati maonekedwe ace a moto; ndi kunyezimira kudamzinga.