Ezekiel 1:28 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuŵalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza m'mitambo tsiku limene kwagwa mvula. Umu ndi m'mene ulemerero wa Chauta unkaonekera. Ndidangoti ntauwona, ndidadzigwetsa pansi chafufumimba, ndipo ndidamva mau ondilankhula.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwake pozungulira pake. Ndiwo maonekedwe a chifaniziro cha ulemerero wa Yehova. Ndipo pakuchipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza mʼmitambo tsiku limene kwagwa mvula. Umu ndi mmene ulemerero wa Yehova umaonekera. Pamene ndinawuona ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akundiyankhula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati maonekedwe a utawaleza uli m'mtambo tsiku la mvula, momwemo maonekedwe a kunyezimira kwace pozungulira pace. Ndiwo maonekedwe a cifaniziro ca ulemerero wa Yehova. Ndipo pakucipenya ndinagwa nkhope pansi, ndipo ndinamva mau a wina wakunena.