Ezekiel 1:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'katikati mwa motowo ndidaona zinthu zokhala ngati zilengolengo zinai. Maonekedwe ake anali otere: thupili mapangidwe ake onga a munthu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi m'kati mwake mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼkatikati mwa motowo munali zinthu zinayi zamaonekedwe a nyama. Thupi lawo limaoneka ngati la munthu
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi m'kati mwace mudaoneka mafaniziro a zamoyo zinai. Ndipo maonekedwe ao ndiwo anafanana ndi munthu,