Ezekiel 1:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Miyendo yake inali yoongoka, koma mapazi ake okhala ndi ziboda zonga za mwanawang'ombe. Zibodazo zinkaŵala ngati mkuŵa wonyezimira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi kumapazi ao kunanga kuphazi kwa mwanawang'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Miyendo yake inali yowongoka; mapazi ake anali a ziboda ngati phazi la mwana wangʼombe. Ndipo zibodazo zinkawala ngati mkuwa wonyezimira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mapazi ao anali mapazi oongoka, ndi ku mapazi ao kunanga kuphazi kwa mwana wa ng'ombe; ndipo ananyezimira ngati mawalidwe a mkuwa wowalitsidwa.