Ezekiel 10:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidayang'ana ku thambo lija lili pamwamba pa mitu ya akerubi, ndipo ndidaona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wokoma wa safiro.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kuthambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a chifaniziro cha mpando wachifumu pamwamba pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine nditayangʼana ku thambo limene lili pamwamba pa mitu ya akerubi ndinangoona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wa mwala wa safiro.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, ku thambo lokhala pamwamba pa mitu ya akerubi kudaoneka ngati mwala wasafiro, ngati maonekedwe a cifaniziro ca mpando wacifumu pamwamba pao.