Ezekiel 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinai. Nkhope yoyamba inali ya kerubi, yachiŵiri inali ya munthu, yachitatu inali ya mkango, yachinai inali ya chiwombankhanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo aliyense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yachiwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yachitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yachinai ndiyo nkhope ya chiombankhanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi. Nkhope yoyamba inali ya Kerubi, nkhope yachiwiri inali ya munthu, nkhope yachitatu inali ya mkango ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ali yense anali nazo nkhope zinai, nkhope yoyamba ndiyo nkhope ya kerubi, ndi nkhope yaciwiri ndiyo nkhope ya munthu, ndi yacitatu ndiyo nkhope ya mkango, ndi yacinai ndiyo nkhope ya ciombankhanga.