Ezekiel 10:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akerubi ankati akamayenda, nayonso mikombero inkayenda m'mbali mwao. Pamene akerubi ankatambasula mapiko ao ndi kuuluka, mikombero inali m'mbali mwao ndithu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakuyenda akerubi, njinga zinayenda pambali pao, ndi pakutambasula mapiko ao akerubiwo kuuluka padziko, njingazi sizinatembenuka pambali pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene akerubi ankayenda, nayonso mikombero ya mʼmbali mwawo inkayenda. Akerubiwo ankati akatambasula mapiko awo kuti auluke mikombero sinkachoka mʼmbali mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakuyenda akerubi, njinga zinayenda pambali pao, ndi pakutambasula mapiko ao akerubiwo kuuluka padziko, njingazi sizinatembenuka pambali pao.