Ezekiel 10:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo Akerubi adatambasula mapiko ao nauluka. Ndidaŵaona akupita, mikombero ili pambali pao. Adakaima pa khomo lakuvuma la Nyumba ya Chauta. Ndipo ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akerubi anatambasula mapiko ao, nauluka padziko, ndili chipenyere, pakuchoka iwo ndi njingazi pa mbali pao; ndipo anaima pa chitseko cha chipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova, ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikuona akerubi, anatambasula mapiko awo ndi kuwuluka. Pamene ankapita, mikombero inapita nawo pamodzi. Akerubi anakayima pa khomo la chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Tsono ulemerero wowala wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akerubi anatambasula mapiko ao, nauluka padziko, ndiri cipenyere, pakucoka iwo ndi njingazi pa mbali pao; ndipo anaima pa citseko ca cipata ca kum'mawa ca nyumba ya Yehova, ndi ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unali pamwamba pao.