Ezekiel 10:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Chauta adauza munthu wovala zabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi, udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa Akerubiwo. Tsono makalawo uŵawaze mu mzinda.” Ndipo ndidamuwona akupitadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wovala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makala a moto ochokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mudzi. Nalowa, ndili chipenyere ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Yehova anawuza munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi. Udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa akerubiwo ndipo uwawaze mu mzinda.” Iye anachita zimenezi ine ndikuona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova analankhula ndi munthu wobvala bafuta, nati, Lowa pakati pa njingazi pansi pa kerubi, nudzaze manja ako makara a moto ocokera pakati pa akerubi, nuwamwaze pamwamba pa mudzi. Nalowa, ndiri cipenyere ine.