Ezekiel 10:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye kuti akerubi adaaimirira ku dzanja lamanja la Nyumba ya Chauta pamene munthuyo ankaloŵa. Ndipo mtambo udaadzaza bwalo lam'kati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsono akerubi anaima kudzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzaza bwalo la m'kati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Apa akerubiwo anali atayima mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu pamene munthuyo ankalowa. Tsono mtambo unadzaza bwalo lamʼkati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsono akerubi anaima ku dzanja lamanja la nyumba polowa munthuyo, ndi mtambo unadzara bwalo la m'kati.