Ezekiel 10:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ulemerero woŵala wa Chauta udachoka pamene udaali, pamwamba pa akerubi, nukafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Tsono Nyumbayo idadzaza ndi mtambo uja, ndipo ulemerero woŵala uja wa Chauta udadzaza bwalo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchokera kukerubi kunka kuchiundo cha nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi cheza cha ulemerero wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pamwamba pa akerubi ndipo unafika ku chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Mtambo unadzaza Nyumba ya Mulungu, ndipo kuwala kwa ulemerero wa Yehova kunadzaza bwalolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kucokera kukerubi kumka ku ciundo ca nyumba; ndi nyumba inadzala nao mtambo, ndi bwalo linadzala ndi ceza ca ulemerero wa Yehova.