Ezekiel 10:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Mulungu adauza munthu wovala zabafuta uja kuti akapale moto pakati pa mikombero, kunsi kwa akerubi. Munthuyo adaloŵa nakaima pambali pa mkombero umodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pomlamulira munthu wovala bafutayo, ndi kuti, Para moto pakati pa njingazi ndi pakati pa akerubi; iye analowa, naima m'mbali mwa njinga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova analamula munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pala moto pakati pa mikombero, pakati pa akerubi.” Munthu uja anapitadi nakayima pa mbali pa mkombero umodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pomlamulira munthu wobvala bafutayo, ndi kuti, Para moto pakati pa njingazi ndi pakati pa akerubi; iye analowa, naima m'mbali mwa njinga.