Ezekiel 10:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pomwepo mmodzi mwa akerubiwo adatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pao. Adapalako motowo, napatsa munthu wovala zabafuta uja. Iyeyo adalandira motowo nkutuluka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo kerubi wina anatambasula dzanja lake pakati pa akerubi kumoto uli pakati pa akerubi, napalako, nauika m'manja mwa iye wovala bafuta, ndiye naulandira, natuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mmodzi wa akerubi anatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pawo. Iye anapalako motowo ndipo anapatsa munthu wovala chovala chabafuta uja. Tsono iye anawulandira natuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo kerubi wina anatambasula dzanja lace pakati pa akerubi ku moto uli pakati pa akerubi, naparako, nauika m'manja mwa iye wobvala bafuta, ndiye naulandita, naturuka.