Ezekiel 10:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidaona mikombero inai pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi. Mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala ya krizoliti.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m'mbali mwa akerubi, njinga imodzi m'mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga ina m'mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine nditayangʼanitsitsa ndinaona mikombero inayi pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi; mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala yokongola ya krizoliti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo ndinapenya, ndipo taonani, njinga zinai m'mbali mwa akerubi, njinga imodzi m'mbali mwa kerubi mmodzi, ndi njinga yina m'mbali mwa kerubi wina, ndi maonekedwe a njingazi ananga mawalidwe a berulo.