Ezekiel 11:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mzimu wa Mulungu udandinyamula kupita nane ku chipata chakuvuma cha Nyumba ya Chauta. Poloŵerapo panali anthu 25, ndipo pakati pa anthuwo ndidaona atsogoleri aŵa a anthu: Yazaniya mwana wa Azuri, ndi Pelatiya mwana wa Benaya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane kuchipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova choloza kum'mawa; ndipo taonani, pa chitseko cha chipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kubwera nane ku chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Kumeneko pa khomo la chipata panali anthu 25, ndipo ndinaona pakati pawo atsogoleri awa: Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane ku cipata ca kum'mawa ca nyumba ya Yehova coloza kum'mawa; ndipo taonani, pa citseko ca cipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.