Ezekiel 11:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ndinkalosa, nthaŵi yomweyo Pelatiya mwana wa Benaya adafa. Tsono ndidadzigwetsa pansi chafufumimba nkufuula kuti, “Inu Ambuye Chauta, kodi mukufuna kuŵatheratu Aisraele onse otsala?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kufuula ndi mau akulu, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu? Mudzatsiriza kodi otsala a Israele?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono pamene ndinkanenera, Pelatiya mwana wa Benaya anafa. Pomwepo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba ndipo ndinafuwula ndi mawu aakulu kuti “Mayo, Ambuye Yehova! Kodi mudzawatheratu Aisraeli onse otsala?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakunenera ine, anamwalira Pelatiya mwana wa Benaya. Pamenepo ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kupfuula ndi mau akuru, ndi kuti, Kalanga ine, Yehova Mulungu! mudzatsiriza kodi otsala a Israyeli?