Ezekiel 11:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Iwe mwana wa munthu, achibale ako, ndiye kuti abale ako, anzako a ku ukapolo, onse a m'banja la Israele, anthu okhala ku Yerusalemu akuŵanena kuti, ‘Onse aja amene adatengedwa ukapolo ali kutali ndi Chauta, dziko lino tsopano nlathu.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako amuna a chibale chako, ndi nyumba yonse ya Israele, yonseyi ndiwo amene okhala m'Yerusalemu ananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale cholowa chathu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wobadwa ndi munthu iwe, abale ako, inde abale ako amuna a cibale cako, ndi nyumba yonse ya Israyeli, yonseyi ndiwo amene okhala m'Yerusalemu ananena nao, Muzikhala kutali kwa Yehova; dziko ili lapatsidwa kwa ife, likhale colowa cathu;