Ezekiel 11:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake uza anzako a ku ukapolo kuti zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndine amene ndidaŵatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuŵabalalitsa ku maiko ambiri. Pakali pano ndikuŵasungabe kumaiko kumene adatengedwako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawachotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi kumaiko adafikako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawacotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi ku maiko adafikako.