Ezekiel 11:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake unene ndithu kuti Ine Chauta mau anga ndikuti, Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuŵasonkhanitsa pamodzi, kuchokera kumaiko kumene ndidaŵabalalitsa. Kenaka ndidzaŵapatsa dziko la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani kumitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani muchoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace uziti, Atero Yehova Mulungu, Ndidzakumemezani ku mitundu ya anthu, ndi kukusonkhanitsani mucoke m'maiko m'mene munabalalikiramo, ndipo ndidzakuninkhani dziko la Israyeli.