Ezekiel 11:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzaŵapatsa mtima watsopano, ndipo ndidzaika moyo watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wouma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzaŵapatsa mtima wofeŵa ngati mnofu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawachotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi, ndi kuika mzimu watsopano m'kati mwao; ndipo ndidzawacotsera mtima wamwala m'thupi mwao, ndi kuwapatsa mtima wamnofu;