Ezekiel 11:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono akerubi aja adayamba kuuluka, mikombero ili m'mbali mwao, ndipo ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pa iwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo akerubi anatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo akerubi anatambasula mapiko ao, ndi njinga zinali pa mbali pao; ndi ulemerero wa Mulungu wa Israyeli unali pamwamba pao.