Ezekiel 11:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ulemerero wa Chautawo udakwera ndi kusiya mzindawo, nukaima pa phiri chakuvuma kwake kwa mzindawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kuchoka pakati pa mudzi, nuima pa phiri la kum'mawa kwa mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ulemerero wa Yehova unakwera kucoka pakati pa mudzi, nuima pa phiri la kum'mawa kwa mudzi.